Nzika zokhudzidwa m’boma la Neno motsogozedwa ndi phungu waku mpoto kwa bomali a Thoko Tembo zalembera kalata mkulu wa bungwe lowona zamiseu kuti ayankhepo pa mfundo zomwe anthuwa anakambirana pa mkumano omwe bungweri linachita ndi adindo am’bomali potsatira ganizo lake losamutsa phula yemwe amayenara kugwira ntchito yokonzera nseu wa Neno.
Malinga ndi kalata yomwe phunguyu walemba ndipo mafumu, makhansala komanso nzika za bomali asainira awuza mkulu wa bungweri kuti ayankhe nkhawa za anthuwa pasanafike lachisanu pa 4 April 2025.
Kalatayi ikufuna bungwe lowona za miseu lilamule kontalakita yemwe akumanga nseu wa Neno kuti ayambe kuthira phula mbali yomwe anamaliza kupala nthawi yogwiritsa ntchito phulayu isanathe.
Kalatayi yomwe aitumizanso kwa nduna ya zamtengatenga komanso bwanamkubwa wa boma la Neno yati ngati bungweri siliyankha pofika lachisanu sabata yamawa, adzamemeza anthu kuti achite zionetsero zosonyeza kusakondwa ndi ganizo la bungweri.
Izi zikudza kutsatira ganizo la bungwe lowona zamiseu lofuna kuti lisamutse migolo ya phula yoposa 2600 yomwe amati agwiritsire ntchito popaka mu nseu wa bomali ndikukagwiritsa ntchito kwina.
Malinga ndi bungweri, phulayu akuyembekezeka kuntha mphamvu pofika mwezi wa June chaka chino.
#NenoFMnews 27 March, 2025