MWANA WA CHAKA CHIMODZI NDI MIYEZI 7 WAFA GALIMOTO ITAMUGUNDA KU NENO

Mwana wa Chaka chimodzi ndi miyezi 7 Dennis Polokera Wafa atamugunda ndi galimoto m’boma la Neno.

Nneneli wa apolisi ku Neno a Rebecca Msoliza wati ngoziyi yachitika madzulo a lachitatu sabata ino.

Iwo ati galimoto ya ntundu wa Toyota Hilux yomwe amayendetsa ndi a Monda Gutachinyundo azaka 47, imachokera mbali yakwa Belo kulowela ku kambale.

Itafika pa Admarc galimotoyo inayima kuti itsitse munthu, atatsika munthuyo dalayivalayo ananyamuka osadziwa kuti pansi pa galimotoyo pali mwana ndipo anamugunda nkuvulala kwambiri m’mutu.

Anthu anatengela mwanayo kuchipatala chachikulu chabomali komwe wamwalira atangofika.

Padakali pano a Monda Gutachinyundo akuwasunga nchitokosi cha apolisi kuyembekezela kukayankha mlandu woyendetsa galimoto mosasamala.

Malemu Dennis Polokera amachokela mmudzi mwa Litchowa kwa mfumu yaikulu Chekucheku m’boma la Neno pomwe a Moda Gitachinyundo amachokela mmudzi mwa Josam kwa mfumu yaikulu Somba ku Blantyre.

Olemba: Jane Chinkwita 27/3/25

Related posts

MCHITIDWE WA ZIWAWA UKUPELEKA MANTHA PA KWA NZIKA ZA DZIKO LINO

MZIKA ZOKHUDZIDWA M’BOMA LA NENO ZAOPSYEZA NRA PA GANIZO LOSAMUTSA PHULA