MCHITIDWE WA ZIWAWA UKUPELEKA MANTHA PA KWA NZIKA ZA DZIKO LINO

Komiti yowona za chitetezo ku nyumba ya malamulo yati kukula kwa mchitidwe wa ziwawa kukupereka chiopsyezo pa chitetezo cha nzika pomwe dziko lino likukonzekera kuchititsa chisankho mwezi wa September chaka chino.

Wapampando wa komitiyi a Salim Bagus ndiye wanena izi lachitatu sabata ino mu mzinda wa Lilongwe, Iye amalankhula utatha mkumano omwe komitiyi inachita ndi mkulu wa polisi mdziko muno Merylin Yolamu.

A Bagus adzudzula apolisi kamba kolekerera anthu achiwembu akuvulaza anthu omwe amkachita zionetsero zabata munzindawu.

Iwo ati apolisi omwe amkagwira ntchito yobweretsa chitetezo panthawiyo akuyenera kuimbidwa mulandu powonerera anthu awupanduwa omwe ananyamula zikwanje nkuvulaza nazo anthu.

Mmau ake mkulu wa polisi a Merlyn Yolamu wavomereza nkhaniyi ponena kuti zinali zolakwikadi kuti apolisi ankangoonerera anthu ochita zionetsero akuwavulaza anthu achiwembuwa.

A Yolamu ati apolisi akuyesetsa kugwira ntchito modzipereka pomwe padakali pano akwanitsa kugwira ena mwa anthu omwe akhala akukhudzidwa ndi mchitidwe wa ziwawa.

Iwo apempha anthu andale ndi magulu ena okhudzidwa kuti athandizane ndi apolisi pofuna kukhwimitsa chitetezo mdziko muno.

Magulu osiyanasiyana akhala akudzudula nthambi ya polisi kamba kolephera kugwira ntchito yawo motsata malamulo.

#Nenofmnews

Related posts

MZIKA ZOKHUDZIDWA M’BOMA LA NENO ZAOPSYEZA NRA PA GANIZO LOSAMUTSA PHULA

MWANA WA CHAKA CHIMODZI NDI MIYEZI 7 WAFA GALIMOTO ITAMUGUNDA KU NENO