CHIWELENGELO CHA ANTHU OPEZEKA NDI TB MMALO OMWELA MOWA CHIKUKWERA M’BOMA LA NENO

Ofesi ya zaumoyo m’boma la Neno yati chiwelengelo cha anthu ochita malonda ndi mmalo omwela mowa omwe akupezeka ndi matenda a chifuwa chachikulu (TB) chakula m’bomali.

Izi anena pamwambo omwe bungwe la la Abwenzi pa zaumoyo linachita lachitatu kumalo omwelako mowa otchedwa ziphaka munsika wa chikonde.

Nkulu owona za matenda achifuwa chachikulu ku ofesi ya zaumoyo mai Maggie Chatuwa ati izi zili chomwechi chifukwa cha ubve komanso kukhala mothinana mmalowa.

Iwo ati ofesi ya zaumoyo ikhazikitsa malo oyezelako matendawa mmadela akumudzi posachedwa pofuna kuchepetsa mtunda omwe anthu amayenda kupita kuchipatala chachikulu kuti akawayeze.

Nkulu owona za matenda a TB ndi HIV Ku bungwe la abwenzi pa zaumoyo a Charles Phiri wati bungweli lachita izi pofuna kupeleka uphungu okhudza matendawa mmalo ochitilako malonda komwe anthu amakhala otanganidwa kuti athe kupewa kufala kwa matendawa.

Wapampando oyang’anila malo ogulitsila ndi kumwela mowa a ziphaka a Lexon Malango wati awonesetsa kuti malowa azikhala aukhondo nthawi zonse.

Iwo apempha khonsolo ya bomali kuti iganizile zomanga zimbuzi zokwanila munsika wa chikonde maka kufupi ndi malo omwela mowa.

Bungwe la abwenzi pa zaumoyo likunka lipeleka mauthenga okhudza matenda a chifuwa chachikulu (TB) pomwe tili mu sabata yolimbikitsa chilungamo popereka thandizo losiyanasiyana la chipatala pa dziko lonse.

Olemba: Jane Chinkwita