Bungwe la atolankhani la media council of Malawi lachititsa maphunzilo a atolankhani ammene angagwirire ntchito munthawi ya zisankho.
Mkulu wa bungweli a Moses Kaufa wati atolankhani azidziwa malamulo ammene angawirire ntchito yawo mu nthawi ya zisankho.
AKaufa apempha atolankhani kulemba nkhani zoona zokhazokha komanso posatengera mbali pamnene tikuyandikira zisankho.
Iwo auza Atolankhani kuti azidziwa komwe angapite akachitidwa chipongwe.
Maphunzilowa amachitikira munzinda wa Blantyre ndi nthandizo la ndalama lochokera Ku National Commission For Unesco.
Wolemba Philadelphia Samera